× Home Files Nkhani MisonkhanoZitsanzoToolsAbout
☰ Menu
Muzisonyeza Kuti Mumadalira Mulungu Mukakumana ndi Anthu Opanda Chidwi mu Utumiki. (th phunziro 20)

Muzisonyeza kuti mudalira Mulungu Mukamakumana ndi Anthu Opanda Chidwi mu utumiki

7 Kodi Yeremiya anakumana ndi mavuto ati ndipo kodi nthawi zina ankamva bwanji?

7 Abale athu ambiri amatumikira m’madera amene amafunika kupirira kwambiri. Mneneri Yeremiya anatumikiranso m’dera lotereli. Iye ankalalikira mu ufumu wa Yuda utatsala pang’ono kuwonongedwa ndipo iyi inali nthawi yovuta kwambiri. Tsiku lililonse chikhulupiriro cha Yeremiya chinkayesedwa chifukwa chomvera Mulungu pogwira ntchito yolalikira uthenga wa chiweruzo Chake. Pa nthawi ina ngakhale Baruki, yemwe anali mlembi wake wokhulupirika, anadandaula chifukwa chotopa. (Yer. 45:2, 3) Kodi Yeremiya anagwa ulesi chifukwa cha zimenezi? Pa nthawi zina iye ankavutika kwambiri maganizo mpaka anafika ponena kuti: “Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!” Ananenanso kuti: “N’chifukwa chiyani ndinabadwa? Kodi ndinabadwa kuti ndidzagwire ntchito yakalavulagaga ndi kukhala wachisoni, ndi kuti moyo wanga ufike kumapeto kwake ndili wamanyazi?” Yer. 20:14, 15, 18.

8 Malinga ndi Yeremiya 17:7, 8 ndi Salimo 1:1-3, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisasiye kubala zipatso zabwino?

8 Koma Yeremiya sanasiye ntchito yake. Iye anapitiriza kudalira Yehova. Zotsatira zake zinali zakuti mneneriyu anaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yehova olembedwa pa Yeremiya 17:7, 8 akuti: “Wodala ndi munthu aliyense amene amakhulupirira Yehova, amene amadalira Yehova. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi. Kutentha kukadzafika iye sadzadziwa, koma masamba ake adzachuluka ndi kukhala obiriwira. Pa nthawi ya chilala sadzada nkhawa kapena kusiya kubalazipatso.”

9 Mofanana ndi mtengo wa zipatso wobiriwira “wobzalidwa m’mphepete mwa madzi” kapena m’munda wa zipatso wothiriridwa bwino, Yeremiya ‘sanasiye kubala zipatso.’ Iye sanalole kufooketsedwa ndi anthu oipa amene ankamunyoza. M’malomwake, iye nthawi zonse ankadalira Kasupe wa “madzi” opatsa moyo ndipo ankatsatira zonse zimene Yehova anamuuza. (Werengani Salimo 1:1-3; Yer. 20:9) Apatu Yeremiya anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri makamaka ngati tikutumikira Mulungu m’madera ovuta. Ngati mukutumikira m’dera lovuta, pitirizani kudalira kwambiri Yehova amene angakuthandizeni kupirira “polengeza dzina lake kwa anthu ena.”Aheb. 13:15.

10 Kodi tili ndi madalitso otanindipo tiyenera kudzifunsa funsoliti?

10 Yehova watipatsa paradaiso wauzimu wokhala ndi zinthu zambiri pofuna kutithandiza kuti tipirire mavuto a pa moyo wathu masiku otsiriza ano. Zina mwa zinthu zimene watipatsa ndi Baibulo lonse, lomwe ndi Mawu ake, ndipo likumasuliridwa molondola m’zinenero zambirimbiri. Iye wapereka chakudya chauzimu chambiri ndiponso pa nthawi yake kudzera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Iye watipatsanso abale ndi alongo amene amatilimbikitsa tikamacheza nawo pa misonkhano yampingo ndi ikuluikulu. Kodi mumagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimene watipatsazi? Anthu onse amene amagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimenezi “adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.” Koma amene samvera Mulungu ‘ adzalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo adzafuula chifukwa chosweka mtima.’ —Yes. 65:13, 14.

MUZISONYEZA KUTI MUMADALIRA MULUNGU MUKAMAKUMANA NDI ANTHU OPANDA CHIDWI MU UTUMIKI

Pa Mat. 28: 19, 20, Yesu anatipatsa lamulo loti tidzilalikira uthenga wabwino kwa anthu amitundu yonse kuti akhale ophunzira ake. Nthawi zina tikamalalikira anthu amamvetsera uthenga wathu pomwe nthawi zina timakumana ndi anthu opanda chidwi.

Kodi anthu opanda chidwi ndi ndani?

Anthu opanda chidwi ndi omwe samalabadira kapena amakana kulandira uthenga wabwino omwe ife timalalikira.Abale athu ambiri amatumikira m'madera omwe amafunika kupilira kwambiri chifukwa cha anthu otsutsa kapena opanda chidwi omwe amakumana nawo mu gawo lawo.

PEMPHERO

Yeremiya anakumananso ndi zimenezi pamene ankalalikira ufumu wa Yuda utatsala pang'ono kuwonongedwa. Anthu ankamutsutsa kwambiri ndipo chikhulupiliro chake chinkayetsedwa tsiku ndi tsiku mpaka anafika poyankhula kuti sadzalankhulanso m'dzina la Yehova (Yer. 20:8)

Sankavutika yekha

Ngakhalenso mlembi wake wokhulupilira Baruki anadandaulanso chifukwa chotopa. (Yer. 45:2, 3) koma Yehova anamulimbikitsa (Yer. 45:5)

MMENE ANALIMBIKITSIDWIRA

Yeremiya anakhuthula nkhawa zake kwa Yehova ndipo ngakhale kuti Baibulo silifotokoza m'mene anamuyankhira, timadziwa kuti Yehova anamuyankha tikamawerenga zomwe analemba pa YEREMIYA 20:9.

Iye anafotokoza kuti mu mtima make mawu a Yehova anali ngati moto woyaka ndipo mawuwo anamuthandiza kupilira kugwira ntchito ya Yehova.

KODI MUKUDZIWA?

Yeremiya analengeza molimba mtima ziweruzo za YEHOVA kwa zaka zoposa 65 ndipo anali odziwika bwino kwambiri m'dziko lonse la Israel chifukwa cholalikira mopanda mantha ndiponso molimba mtima. Patatha zaka pafupifupi 600 kuchokera nthawi imeneyo anthu ena ankati Yeremiya wauka ataona m'mene Yesu ankalankhulira molimba mtima. (Mat. 16:13, 14) Zinatheka bwanji? Mawu a Yehova anampatsa mphamvu ndipo anamulimbitsa mtima kuti azilalikira.

KODI TIYENERA KUTANI?

Ifenso tizipitiriza kudalira kwambiri Yehova amene angatithandize kupilira, polengeza dzina lake matsiku ano.

KUSINKHASINKHA

SALIMO 1:1-3

Monga momwe mtengo wa zipatso wobiliwira, wozalidwa mphepete mwa madzi (kapena kuti munda othililidwa bwino / osasowa madzi) umapitilizira kubereka zipatso, tisamalole kufooketsedwa ndi anthu oipa omwe angamatinyoze. Mmalomwake, nthawi zonse tizidalira kasupe wa madzi opatsa moyo ndipo tizitsatira zonse zomwe Yehova amatiuza.

PARADAISO WAUZIMU

Monga mmene paradaiso wakuthupi azakhalire otsangalatsa ndi wamtendere, Yehova watipatsa paradaiso wauzimu kuti tizitha kupilira mavuto omwe tikukumana nawowa kwinaku tikupitirizabe kulalikira uthenga wabwino, m'matsiku otsiriza ano:

  • baibulo lomwe ndi mawu ake ndpo likupezeka pafupifupi mchinenero chilichonse
  • chakudya chambiri ndi cha pa nthawi yake chomwe timapatsidwa kudzera mwa kapolo
  • abale ndi alongo omwe amatilimbikitsa tikakumana ndi vuto kapenanso tikamacheza nawo pa misonkhano.TIYENERA KUTANI?

    Tiyenera kumagwiritsa ntchito mokwanira zomwe tapatsidwazi kuti tikhale ngati mtengo odzalidwa mphepete mwa mtsinje omwe sumasiya kubala zipatso.

    KODI TAKAMBIRANA ZOTANI?

    Choncho tiyeni tonse tizisonyeza kuti timadalira Yehova tikamakumana ndi anthu opanda chidwi mu utumiki.


    online: | hits: x

    Back to top

    “M'patseni Yehova ulemelero
    woyenera dzina lake.”
       - Salimo 96:8.