×
Home Files Nkhani MisonkhanoZitsanzoToolsAbout
Kodi mumayendera maganizo a ndani?

KODI MUMAYENDERA MAGANIZO A NDANI? ^

Satana amagwiritsa ntchito chuma ngati nsampha kwa atumiki a Yehova. (Miyambo 23: 4, 5) Ngakhale kuti Yobu anali ndi chuma chambiri, sanalole kuti chimulepheretse kukhulupilika kwa Yehova. Iye anadalirabe Yehova ngakhale pamene chumachao chinatha ( Yobu 1:13-19) ndipo sanapitirize kuchifunafuna.

TINGATANI KUTI TIZIYENDERA MAGANIZO A YEHOVA? ^

  1. Tidziika Ufumu wa Mulungu pa malo oyamba (Mateyu 5:3;; 6:33)

    Amene amatsatira mzimu wa dziko (Satana), amaputsitsidwa ndipo alibe chiyembekezo. Yesu anapereka chitsanzo cha munthu yemwe anali ndi chuma yemwe ankati "moyo wanga sangalala". Tikamatsatira mfundo za Yehova, zimatithandiza kukhala ndi mtendere wa mumtima ndipo timakhala mosangalala ndi abale ndi alongo athu. (Yohane 4:34; Miyambo 3:1; Mika 6:8; Afilipi 4: 5-7)

  2. Tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake. 1 Akorinto 2: 14-16)

    Timayamikira chifukwa timadziwitsidwa za dzina la Yehova (Salimo 16:11) Nthawi zonse malangiza a Yehova amathandiza ndipo samatipunthwitsa.



Back to top

“M'patseni Yehova ulemelero
woyenera dzina lake.”
   - Salimo 96:8.